Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 8:25-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo anatenga mafutawo ndi mcira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ace, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

26. ndipo mu mtanga wa mkate wopanda cotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

27. anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ace amuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

28. Pamenepo Mose anazicotsa ku manja ao, nazitentha pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

29. Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.

30. Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zobvala zace, ndi pa ana ace amuna, ndi pa zobvala za ana ace amuna omwe; napatula Aroni, ndi zobvala zace, ndi ana ace amuna, ndi zobvala za ana ace amuna omwe.

31. Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna, Phikani nyamayi pakhomo pa cihema cokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu mtanga wa nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ace aidye.

32. Koma cotsalira ca nyama ndi mkate mucitenthe ndi moto.

33. Ndipo musaturuka pa khomo la cihema cokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.

34. Monga anacita lero lino, momwemo Yehova anauza kucita, kukucitirani cotetezera.

35. Ndipo mukhale pakhomo pa cihema cokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga cilangizo ca Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.

36. Ndipo Aroni ndi ana ace amuna anacita zonse zimene Yehova anauza pa dzanja la Mose.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 8