Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 8:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.

19. Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

20. Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zace; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.

21. Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

22. Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ace amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo.

23. Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wace naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa cala cacikuru ca ku dzanja lamanja lace, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja.

24. Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa cala cacikuru ca ku dzanja lamanja lao, ndi pacala cacikuru ca phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira,

25. Ndipo anatenga mafutawo ndi mcira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ace, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

26. ndipo mu mtanga wa mkate wopanda cotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

27. anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ace amuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

28. Pamenepo Mose anazicotsa ku manja ao, nazitentha pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zocita pfungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

29. Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.

30. Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zobvala zace, ndi pa ana ace amuna, ndi pa zobvala za ana ace amuna omwe; napatula Aroni, ndi zobvala zace, ndi ana ace amuna, ndi zobvala za ana ace amuna omwe.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 8