Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 7:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumcembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi paciwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo,

10. Ndipo nsembe zonse zaufa zosanganiza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.

11. Ndipo cilamulo ca nsembe zoyamika, zimene azibwera Daze kwa Yehova ndi ici:

12. akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndinsembe yolemekeza, timitanda topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda cotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tooca, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta.

13. Abwere naco copereka cace pamodzi ndi timitanda ta mkate wacotupitsa, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, ya nsembe zoyamika zace.

14. Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika.

15. Kunena za nyama ya nsembe volemekeza ya nsembe zoyamika zace, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa.

16. Koma nsembe ya copereka cace ikakhala ya cowinda, kapena copereka caufuhi, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yace; ndipo m'mawa adye cotsalirapo;

17. koma cotsalira pa nyama ya nsembeyo tsiku lacitatu, acitenthe.

18. Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zace tsiku lacitatu, sikubvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo cinthu conyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 7