Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 5:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. ndipo kudzali, ataparamula cimodzi ca izi, aziulula cimene adacimwa naco;

6. nadze nayo nsembe yoparamula kwa Yehova cifukwa ca kulakwa kwace adacimwira, ndiyo msoti wa nkhosa, kapena msoti wa mbuzi, ukhale nsembe yaucimo; ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa kwace.

7. Ndipo cuma cace cikapanda kufikira nkhosa, wocimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yace yoparamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yaucimo, ndi yina ya nsembe yopsereza.

8. Ndipo adze nazo kwa wansembe, ndiye ayambe kubwera nayo ija ya kwa nsembe yaucimo, napotole mutu wace pakhosi pace, osaucotsa;

9. nawazeko mwazi wa nsembe yaucimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yaucimo.

10. Ndipo aikonze inzace ikhale nsembe yopsereza, manga mwa lemba lace; ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa adacimwira, ndipo adzakhululukidwa.

11. Koma cuma cace cikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wocimwayo azidza naco copereka cace limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yaucima; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo libona ai; pakuti ndico nsembe yaucimo.

12. Ndipo adze naco kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe monga umo amacitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yaucimo.

13. Ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa kwace adacimwira cimodzi ca izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo cotsalira cikhale ca wansembe, monga umo amacitira copereka caufaco.

14. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

15. Munthu akacita mosakhulupirika, nakacimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema, ya m'gulu lace, monga umayesa mtengo wace pochula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yoparamula;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 5