Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 5:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo adze naco kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe monga umo amacitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yaucimo.

13. Ndipo wansembe amcitire comtetezera cifukwa ca kucimwa kwace adacimwira cimodzi ca izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo cotsalira cikhale ca wansembe, monga umo amacitira copereka caufaco.

14. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

15. Munthu akacita mosakhulupirika, nakacimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema, ya m'gulu lace, monga umayesa mtengo wace pochula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yoparamula;

16. ndipo abwezere colakwira copatulikaco, naonjezepo limodzi la magawo asanu, napereke kwa wansembe; ndi wansembeyo amcitire comtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yoparamula; ndipo adzakhululukidwa.

17. Ndipo munthu akacimwa, nakacita dna ca zinthu ziti zonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma waparamula, azisenza mphulupulu yace.

18. Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda cirema ya m'khola lace, monga umayesa mtengo wace, ikhale nsembe yoparamula; ndipo wansembeyo amcitire comtetezera cifukwa ca kusacimwa dala kwace, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa.

19. Iyo ndiyo nsembe yoparamula; munthuyu anaparamula ndithu pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 5