Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 23:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza naco copereka ca Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse.

15. Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wa nsembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu;

16. muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lacisanu ndi ciwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.

17. Muturuke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi cotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.

18. Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, ana a nkhosa asanu ndi awiri, opanda cirema a caka cimodzi, ndi ng'ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.

19. Mukonzenso mwana wa mbuzi mmodzi akhale nsembe yaucimo, ndi ana a nkhosa awiri a caka cimodzi akhale nsembe yoyamika.

20. Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi ana a nkhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.

21. Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.

22. Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.

23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

24. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko cikumbutso ca kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.

25. Musamagwira nchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.

26. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Levitiko 23