Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi ana a nkhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.