Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 16:12-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makara amoto, kuwacotsa pa guwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ace odzala ndi cofukiza copera ca pfungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsaru yocinga;

13. naike cofukizaco pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa cofukiza ciphimbe cotetezerapo cokhala pamboni, kuti angafe.

14. Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi cala cace pacotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi cala cace cakuno ca cotetezerapo kasanu ndi kawiri.

15. Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yaucimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wace m'tseri mwa nsaru yocinga, nacite nao mwazi wace monga umo anacitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pacotetezerapo ndi cakuno ca cotetezerapo;

16. nacitire cotetezera malo opatulika, cifukwa ca kudetsedwa kwa ana a Israyeli, ndi cifukwa ca zolakwa zao, monga mwa zocimwa zao zonse; nacitire cihema cokomanako momwemo, cakukhala nao pakati pa zodetsa zao.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 16