Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 15:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo munthu ali yense akakhudza kanthu kali konse kadali pansi pace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

11. Ndipo munthu ali yense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

12. Ndipo zotengera zadothi wazikhudza wakukhayo, aziphwanye; ndi zamtengo, azitsuke ndi madzi.

13. Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwace, natsuke zobvala zace; nasambe thupi lace ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.

14. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la cihema cokomanako, nazipereke kwa wansembe;

15. ndipo wansembe azipereke izo, imodzi ikhale nsembe yaucimo, ndi yina nsembe yopsereza; ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova cifukwa ca kukha kwace.

16. Ndipo munthu ali yense akagona uipa, azisamba thupi lace lonse ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

17. Ndipo cobvala ciri conse, ndi cikopa ciri conse, anagona uipa pamenepo azitsuke ndi madzi, nizidzakhala zodetsedwa kufikira madzulo.

18. Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 15