Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwace, natsuke zobvala zace; nasambe thupi lace ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.