Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 15:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mose ndi Aroni, nati,

2. Nenani nao ana a Israyeli, nimuti nao, Pamene mwamuna ali yense ali ndi nthenda yakukha m'thupi mwace, akhale wodetsedwa, cifukwaca kukha kwace.

3. Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwace ndiko: ngakhale cakukhaco cituruka m'thupi mwace, ngakhale caleka m'thupi mwace, ndiko kumdetsa kwace.

4. Kama ali yense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi cinthu ciri conse acikhalira ciri codetsedwa.

5. Ndipo munthu ali yense wakukhudza kama wace azitsuka zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo,

6. Ndipo iye wakukhalira cinthu ciri conse adacikhalira wakukhayo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

7. Ndipo iye wakukhudza thupi la uyo wakukhayo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

8. Ndipo wakukhayo akalabvulira wina woyera; pamenepo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

9. Ndipo mbereko iri yonse akwerapo wakukhayo iri yodetsedwa.

10. Ndipo munthu ali yense akakhudza kanthu kali konse kadali pansi pace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

11. Ndipo munthu ali yense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

12. Ndipo zotengera zadothi wazikhudza wakukhayo, aziphwanye; ndi zamtengo, azitsuke ndi madzi.

13. Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwace, natsuke zobvala zace; nasambe thupi lace ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 15