Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 14:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lace, namuche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.

8. Ndipo iye wakutiayeretsedwe atsuke zobvala zace, namete tsitsi lace lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kucigono, koma agone pa bwalo la hema wace masiku asanu ndi awiri.

9. Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lace lonse la pamutu pace, ndi ndebvu zace, ndi nsidze zace, inde amete tsitsi lace lonse; natsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, nakhale woyera.

10. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge ana a nkhosa awiri, amuna opanda cirema, ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamkazi wa caka cimodzi wopanda cirema, ndi atatu a magawo khumi a ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa mafuta.

11. Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako;

12. ndipo wansembe atenge mwana wa nkhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yoparamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

13. Ndipo akaphere mwana wa nkhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yaucimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yaucimo momwemo nsembe yoparamula, nja wansembe; ndiyo yopatulikitsa.

14. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yoparamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja;

15. ndipo wansembe atengeko muyeso wa mafuta, nawathire pa cikhato ca dzanja lace lamanzere la iye mwini;

16. ndipo wansembe abviike cala cace ca dzanja lace lamanja ca iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lace lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi cala cace pamaso pa Yehova;

17. ndipo wansembe apakeko mafuta okh a ria m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yoparamula;

18. natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lace la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amcitire comtetezers pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 14