Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 13:23-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Koma ngati cikanga caima pomwepo, cosakula, ndico cipsera ca cironda; ndipo wansembe amuche woyera.

24. Kapena pamene thupi lidapsya ndi mota pakhungu pace, ndipo mnofu wofiira wakupsyawo usanduka cikanga cotuuluka, kapena cotuwa:

25. pamenepo wansembe acione; ndipo taonani, ngati tsitsi la cikanga lasanduka lotuwa, ndipo cioneka cakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsyamo; ndipo wansembe azimucha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.

26. Koma akaonapo wansembe, ndipo taonani, mulibe tsitsi loyera m'cikangamo, ndipo sicikumba kubzola khungu, koma cazimba; pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

27. ndipo wansembe amuone tsiku lacisanu ndi ciwiri; ngati cakula pakhungu, wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate,

28. Ndipo ngati cikanga ciima pomwepo, cosakula pakhungu koma cazimba; ndico cotupa ca kupsya; ndipo wansembe amuche woyera; pakuti ndico cipsera ca kupsya.

29. Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi nthenda pamutu kapena pandebvu,

30. wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndebvu.

31. Ndipo wansembe akaona nthenda yamfundu, ndipo taonani, ioneka yosakumba kubzola khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda pamenepo, wansembe ambindikiritse iye ali ndi mfundu masiku asanu ndi awiri;

32. ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu,

33. pamenepo azimeta, koma osameta pamfundu; ndipo wansembe ambindikiritse iye wamfundu masiku asanu ndi awiri ena;

34. ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amuche woyera, ndipo iye atsuke zobvala zace, nakhala woyera.

35. Koma ngati mfundu ikula pakhungu atachedwa woyera;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 13