Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 48:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Israyeli anatambalitsa dzanja lace lamanja, naliika pa mutu wa Efraimu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lace lamanzere pa mutu wa Manase anapingasitsa manja ace dala; cifukwa Manase anali woyamba.

15. Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pace anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isake, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,

16. mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa lichulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isake; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi.

17. Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wace anaika dzanja lace lamanja pa mutu wa Efraimu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wace, kulicotsa pa mutu wa Efraimu ndi kuliika pa muta wa Manase.

18. Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Msatero atate wanga, cifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wace.

19. Koma anakana atate wace, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; Iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwace adzakhala wamkuru ndi iye, ndipo mbeu zace zidzakhala mitundu yambirimbiri.

20. Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israyeli adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efraimu ndi monga Manase; ndipo anaika Efraimu woyamba wa Manase.

21. Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Taona, ndirinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.

22. Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.

Werengani mutu wathunthu Genesis 48