Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 48:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ace amuna awiri, Manase ndi Efraimu, apite naye.

2. Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Yakobo anadzilimbitsa, nakhala tsonga pakama.

3. Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, a Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,

4. Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakucurukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao cikhalire.

5. Tsopano ana ako amuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Aigupto, ndisanadze kwa iwe ku Aigupto, ndiwo anga; Efraimu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.

6. Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awaphe dzina la abale ao m'colowa cao.

7. Tsono ine, pamene ndinacokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efrati; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efrati (ndiwo Betelehemu).

8. Ndipo Israyeli anayang'ana ana amuna a Yosefe, nati, Ndani awa?

9. Ndipo Yosefe anati kwa atate wace, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.

10. Koma maso a Israyeli anali akhungu m'ukalamba wace, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.

11. Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndione nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.

12. Ndipo Yosefe anaturutsa iwo pakati pa maondo ace, nawerama ndi nkhope yace pansi.

13. Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efraimu m'dzanja lace lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lace lamanzere ku dzanja lamanja la Israyeli, nadza nao pafupi ndi iye.

14. Ndipo Israyeli anatambalitsa dzanja lace lamanja, naliika pa mutu wa Efraimu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lace lamanzere pa mutu wa Manase anapingasitsa manja ace dala; cifukwa Manase anali woyamba.

Werengani mutu wathunthu Genesis 48