Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 41:42-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo Farao anacotsa mphete yosindikizira yace pa dzanja lace, naibveka pa dzanja la Yosefe, nambveka iye ndi zobvalira zabafuta, naika unyolo wagolidi pakhosi pace;

43. ndipo anamkweza iye m'gareta wace waciwiri amene anali naye: ndipo anapfuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Aigupto,

44. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu ali yense adzatukula dzanja lace kapena mwendo wace m'dziko lonse la Aigupto.

45. Ndipo Farao anamucha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anaturuka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Aigupto.

46. Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aigupto, Ndipo Yosefe anaturuka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Aigupto,

47. Ndipo zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri.

48. Ndipo anasonkhanitsa cakudya conse ca zaka zisanu ndi ziwiri cimene cinali m'dziko la Aigupto, nasunga cakudyaco m'midzi; cakudya ca m'minda, yozinga midzi yonse, anacisunga m'menemo.

49. Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mcenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; cifukwa anali wosawerengeka.

50. Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana amuna awiri, cisanafike caka ca njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Porifera wansembe wa Oni anambalira iye.

51. Ndipo Yosefe anamucha dzina la woyamba Manase, cifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zobvuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.

52. Ndipo dzina la waciwiri anamucha Efraimu: cifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.

53. Ndipo zaka zakucuruka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Aigupto, zinatha.

54. Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Aigupto munali cakudya.

55. Ndipo pamene dziko lonse la Aigupto linali ndi njala, anthu anapfuulira Farao awapatse cakudya; ndipo Farao anati kwa Aaigupto onse, Pitani kwa Yosefe: cimene iye anena kwa inu citani.

56. Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aaigupto: ndipo njala inakula m'dziko la Aigupto.

57. Ndipo maiko onse anafika ku Aigupto kudzagula tirigu kwa Yosefe: cifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 41