Ndipo Farao anamucha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anaturuka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Aigupto.