Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 38:3-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Eri.

4. Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Onani.

5. Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namucha dzina lace Sela: ndipo iye anali pa Kezibi pamene mkazi anambala iye,

6. Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wace woyamba mkazi, ndipo dzina lace ndilo Tamara.

7. Koma Eri mwana wace woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye.

8. Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumcitira mkazi zoyenera mphwace wa mwamuna wace, ndi kumuukitsira mkuru wako mbeu.

9. Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yace: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wace, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkuru wace.

10. Koma cimene iye anacita cinali coipa pamaso pa Mulungu, ndipo anamupha iyenso.

11. Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpengozi wace, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna; cifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ace. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wace.

12. Atacuruka masiku mwana wamkazi wa Sua, mkazi wace wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zace ku Timna, iye ndi bwenzi lace Hira, M-adulami.

13. Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zace.

14. Pamenepo anabvula zobvala zacezamasiye, nadzipfundandi copfunda cace, nabvala nakhala pa cipata ca Enaimu, cifukwa ciri pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatsa iye kuti akhale mkazi wace.

15. Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: cifukwa iye anabisa nkhope yace.

16. Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; cifukwa sanamdziwa kuti ndiye mpongozi wace. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine ciani kuti ulowane ndi ine.

Werengani mutu wathunthu Genesis 38