Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 37:20-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi cirombo; ndipo tidzaona momwe adzacita maloto ace.

21. Ndipo Rubeni anamva nampulumutsa iye m'manja mwao; nati, Tisamuphe iye,

22. Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'cipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye ra'manja mwao, ambwezenso kwa atate wace.

23. Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ace, anambvula Yosefe malaya ace, malaya amwinjiro amene anabvala iye;

24. ndipo anamtenga iye, namponya m'dzenjemo; m'dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m'menemo.

25. Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye cakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismayeli anacokera ku Gileadi ndi ngamila zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano alinkumuka kutsikira nazo ku Aigupto.

26. Ndipo Yuda anati kwa abale ace, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wace?

27. Tiyeni timgulitse iye kwa Aismayeli, tisasamulire iye manja; cifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ace.

28. Ndipo ana pita pamenepo Amidyani a malonda: ndipo anamturutsa namkweza Yosefem'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismayeli ndi ndalama zasiliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Aigupto.

29. Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsaru yace.

30. Ndipo anabwera kwa abale ace, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti?

31. Ndipo anatenga malaya ace a Yosefe, napha tonde, nabvika malaya m'mwazi wace:

32. natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.

33. Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi cirombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.

34. Yakobo ndipo anang'amba malaya ace, nabvala ciguduli m'cuuno mwace namlirira mwana wace masiku ambiri.

35. Ndipo ana amuna ace onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wace ndipo anamlirira.

36. Amidyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Aigupto kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.

Werengani mutu wathunthu Genesis 37