Ndipo ana amuna ace onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wace ndipo anamlirira.