Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 37:2-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mibadwo ya Yakobo ndi iyi: Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ace; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wace; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wace mbiri yao yoipa.

3. Koma Israyeli anamkonda Yosefe koposa ana ace onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wace; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro.

4. Ndipo abale ace anaona kuti atate wace anamkonda iye koposa abale ace onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.

5. Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ace; ndipo anamuda iye koposa.

6. Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota:

7. pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima ciriri! ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.

8. Abale ace ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? ndipo anamuda Iye koposa cifukwa ca maloto ace ndi mau ace.

9. Ndipo analotanso lata lina, nafotokozera abale ace, nati, Taonani, ndalotanso lata lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.

10. Ndipo iye anafotokozera atate wace ndi abale ace; ndipo atate wace anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi?

11. Ndipo abale ace anamcitira iye nsanje, koma atate wace anasunga mau amene m'mtima mwace.

12. Ndipo abale ace ananka kukaweta zoweta za atate wao m'Sekemu.

13. Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta m'Sekemu? tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.

14. Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta ziri bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kucokera m'cigwa ca Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.

15. Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m'thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna ciani?

16. Ndipo iye anati, Ndifuna abale anga. Undiuzetu kumene adyetsa zoweta.

17. Munthuyo ndipo anati, Anacoka pano; pakuti ndinamva alinkuti, Timuke ku Dotana. Yosefe ndipo anatsata abale ace, nawapeza ali ku Dotana.

Werengani mutu wathunthu Genesis 37