Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 37:12-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo abale ace ananka kukaweta zoweta za atate wao m'Sekemu.

13. Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta m'Sekemu? tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.

14. Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta ziri bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kucokera m'cigwa ca Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.

15. Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m'thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna ciani?

16. Ndipo iye anati, Ndifuna abale anga. Undiuzetu kumene adyetsa zoweta.

17. Munthuyo ndipo anati, Anacoka pano; pakuti ndinamva alinkuti, Timuke ku Dotana. Yosefe ndipo anatsata abale ace, nawapeza ali ku Dotana.

18. Ndipo iwo anamuona iye ali patari, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye ciwembu kuti amuphe.

19. Ndipo anati wina ndi mnzace, Taonani, alinkudza mwini maloto uja.

20. Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi cirombo; ndipo tidzaona momwe adzacita maloto ace.

21. Ndipo Rubeni anamva nampulumutsa iye m'manja mwao; nati, Tisamuphe iye,

22. Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'cipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye ra'manja mwao, ambwezenso kwa atate wace.

23. Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ace, anambvula Yosefe malaya ace, malaya amwinjiro amene anabvala iye;

24. ndipo anamtenga iye, namponya m'dzenjemo; m'dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m'menemo.

25. Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye cakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismayeli anacokera ku Gileadi ndi ngamila zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano alinkumuka kutsikira nazo ku Aigupto.

26. Ndipo Yuda anati kwa abale ace, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wace?

27. Tiyeni timgulitse iye kwa Aismayeli, tisasamulire iye manja; cifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 37