Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 36:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi:

2. Esau anatenga akazi ace a ana akazi a m'Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Mhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibeoni Mhivi;

3. ndi Basemati mwana wamkazi wa lsmayeli, mlongo wace wa Nabayoti.

4. Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reueli;

5. ndipo Oholibama anabala Jeusi, ndi Jalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana amuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani.

6. Ndipo Esau anatenga akazi ace, ndi ana ace amuna, ndi ana ace akazi, ndi anthu onse a m'banja mwace, ndi ng'ombe zace, ndi zoweta zace, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patari ndi Yakobo mphwace.

7. Cifukwa cuma cao cinali cambiri cotero kuti sanakhoza kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira cifukwa ca ng'ombe zao.

8. Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu.

9. Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi:

10. amenewa ndi maina a ana amuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wace wa Esau, Reueli mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wace wa Esau.

11. Ndipo ana amuna a Elifazi ndiwo Temani, Omari, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi.

12. Ndipo Timna anali mkazi wace wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleki: amenewa ndi ana amuna a Ada mkazi wace wa Esau.

13. Ndi ana amuna a Reueli: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; amenewa ndi ana a Basemati mkazi wace wa Esau.

14. Ana amuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibeoni, mkazi wace wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Jeusi, ndi Jalamu, ndi Kora.

15. Amenewa ndi mafumu a ana amuna a Esau: ana amuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omari, mfumu Zefo, mfumu Kenazi,

16. mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleki: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana amuna a Ada.

Werengani mutu wathunthu Genesis 36