Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 30:32-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse ndi kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathotho-mathotho ndi zamaanga-maanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamaangamaanga ndi zamathotho-mathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

33. Cotero cilungamo canga cidzandibvomereza m'tsogolomo, pamene udzandifika cifukwa ca malipiro amene ali patsogolo pako; iri yonse yosakhala yamathotho-mathotho ndi yamaanga-maanga ya mbuzi, ndi iri yonse ya mbuzi yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

34. Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.

35. Tsiku lomwelo Labani anacotsa atonde amene anali amipyololo-mipyololo ndi amathotho-mathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamaanga-maanga ndi zamathotho-mathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ace amuna.

36. Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani.

37. Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wowisi walibne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo.

Werengani mutu wathunthu Genesis 30