Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 30:20-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopane mwamuna wanga adzakhala ndi ine, cifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamucha dzina lace Zebuloni.

21. Pambuyo pace ndipo anabala mwana wamkazi, namucha dzina lace Dina.

22. Ndipo Mulungu anakumbukila Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwace.

23. Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wacotsa manyazi anga;

24. namucha dzina lace Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina.

25. Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.

26. Undipatse ine akazi anga ndi ana anga cifukwa ca iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: cifukwa udziwa iwe nchito imene ndinakugwirira iwe.

27. Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, cifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine cifukwa ca iwe.

28. Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa.

29. Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe comwe ndakutumikira iwe ndi comwe zacita zoweta zako ndi ine.

30. Cifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zacuruka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kuli konse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?

31. Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandicitira ine cotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.

32. Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse ndi kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathotho-mathotho ndi zamaanga-maanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamaangamaanga ndi zamathotho-mathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.

33. Cotero cilungamo canga cidzandibvomereza m'tsogolomo, pamene udzandifika cifukwa ca malipiro amene ali patsogolo pako; iri yonse yosakhala yamathotho-mathotho ndi yamaanga-maanga ya mbuzi, ndi iri yonse ya mbuzi yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

34. Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.

35. Tsiku lomwelo Labani anacotsa atonde amene anali amipyololo-mipyololo ndi amathotho-mathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamaanga-maanga ndi zamathotho-mathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ace amuna.

36. Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani.

Werengani mutu wathunthu Genesis 30