Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 29:21-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse Ine mkazi wanga, cifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.

22. Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero.

23. Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wace wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo.

24. Ndipo Labani anampatsa mwana wace wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wace kuti akhale mdzakazi wa Leya.

25. Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Ciani wandicitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe cifukwa ca Rakele? wandinyenga ine bwanji?

26. Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng'ono asanapatse wamkuru.

27. Umarize sabata lace la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso cifukwa ca utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri.

28. Yakobo ndipo anacita cotero namariza sabata lace; ndipo Labani anampatsa iye Rakele mwana wace wamkazi kuti akwatire iyenso.

29. Ndipo Labani anampatsa mwana wace wamkazi Rakele Biliha mdzakazi wace kuti akhale mdzakazi wa Rakele.

30. Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso.

31. Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leva, anatsegula m'mimba mwace; koma Rakele anali wouma.

32. Ndipo Leyaanatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Rubeni; pakuti anati, Cifukwa kuti tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.

33. Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Cifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamucha dzina lace Simeoni.

34. Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine cifukwa ndambalira iye ana amuna atatu; cifukwa cace anamucha dzina lace Levi.

35. Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; cifukwa cace anamucha dzina lace Yuda; pamenepo analeka kubala.

Werengani mutu wathunthu Genesis 29