Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 24:6-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Cenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko.

7. Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; iye adzatumiza mthenga wace akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.

8. Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosacimwa pa cilumbiro cangaci: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko.

9. Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lace pansi pa ncafu yace ya Abrahamu mbuye wace, namlumbirira iye za cinthuco.

10. Ndipo mnyamatayo anatenga ngamila khumi za mbuyace, namuka: cifukwa kuti cuma conse ca mbuyace cinali m'dzanja lace: ndipo anacoka namuka ku Mesopotamiya, ku mudzi wa Nahori.

11. Ndipo anagwaditsa ngamila zace kunja kwa mudzi, ku citsime ca madzi nthawi yamadzulo, nthawi yoturuka akazi kudzatunga madzi.

12. Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumcitire ufulu mbuyanga Abrahamu,

13. Taonani, ine ndiima pa citsime ca madzi; ndipo ana akazi a m'mudzi aturuka kudzatunga madzi;

14. ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo cotero ndidzadziwa kuti mwamcitira mbuyanga ufulu.

15. Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anaturuka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwace wa Abrahamu, ndi mtsuko wace paphewa pace.

16. Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ace, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wace, nakwera.

17. Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako.

18. Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m'manja mwace namwetsa iye.

19. Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse.

20. Ndipo anafulumira nathira madzi a m'mtsuko wace m'comwera, nathamangiranso kucitsime kukatunga, nazitungira ngamila zace zonse.

Werengani mutu wathunthu Genesis 24