Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 13:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova.

5. Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema.

6. Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: cifukwa kuti cuma cao cinali cambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.

7. Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperezi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.

8. Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisacite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: cifukwa kuti ife ndife abale.

9. Dziko lonse siliri pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.

10. Ndipo Loti anatukula maso ace nayang'ana cigwa conse ca Yordano kuti conseco cinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Aigupto pakunka ku Zoari.

11. Ndipo Loti anasankha cigwa conse ca Yordano; ndipo Loti anacoka ulendo wace kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzace.

12. Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'midzi ya m'cigwa, nasendeza hema wace kufikira ku Sodomu.

13. Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ocimwa kwambiri pamaso pa Yehova.

14. Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwela, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo:

15. cifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.

Werengani mutu wathunthu Genesis 13