Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 1:13-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacitatu.

14. Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

15. zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi; ndipo kunatero.

16. Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikuru ziwiri; counikira cacikuru cakulamulira usana, counikira cacing'ono cakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

17. Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi,

18. nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabino.

19. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacinai.

20. Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zocuruka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga.

21. Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikuru ndi zoyendayenda zamoyo zakucuruka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wace: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

22. Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zicuruke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zicuruke pa dziko lapansi.

23. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu.

24. Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.

Werengani mutu wathunthu Genesis 1