Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 5:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Limodzi la magawo ace atatu utenthe ndi moto pakati pa mudzi pakutha masiku a kuzingidwa mudzi, nutenge gawo lina ndi kukwapula-kwapula ndi lupanga pozungulira pace, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.

3. Utengekonso owerengeka ndi kuwamanga m'mkawo wa maraya ako.

4. Nutengekonso pa amenewa ndi kuwaponya pakati pa moto, ndi kuwatentha m'moto; kucokera kumeneko udzaturuka moto pa nyumba yonse ya Israyeli.

5. Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati pa amitundu, ndi pozungulira pace pali maiko.

6. Koma anakaniza maweruzo anga ndi kucita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendamo.

7. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawacita;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 5