Koma anakaniza maweruzo anga ndi kucita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendamo.