Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 47:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Nditabwera tsono, taonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri tsidya lino ndi lija.

8. Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa aturukira ku dera la kum'mawa, natsikira kucidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ace.

9. Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zocuruka zidzakhala ndi moyo kuti konse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzacuruka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m'nyanja; ndipo kuli konse mtsinje ufikako ziri zonse zidzakhala ndi moyo.

10. Ndipo kudzacitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Eneglaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundu mitundu, ngati nsomba za m'nyanja yaikuru, zambirimbiri.

11. Koma pali matope ace ndi zithaphwi zace sipadzakonzeka, paperekedwa pakhale pamcere.

12. Ndipo kumtsinje, kugombe kwace tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uli wonse wa cakudya, osafota tsamba lace, zipatso zace zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ace atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zace zidzakhala cakudya, ndi tsamba lace lakuciritsa.

13. Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale colowa cao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 47