Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 46:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipataco, kunja kwace, naime ku nsanamira ya cipata; ndipo ansembe akonze nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, nalambire iye ku ciundo ca cipata; atatero aturuke; koma pacipata pasatsekedwe mpaka madzulo.

3. Ndipo anthu a m'dziko alambire pa citseko ca cipata ici pamaso pa Yehova pamasabata, ndi pokhala mwezi.

4. Ndipo nsembe yopsereza imene kalonga azipereka kwa Yehova pa Sabata ndiyo ana a nkhosa asanu ndi mmodzi opanda cirema, ndi nkhosa yamphongo yopanda cirema,

5. ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini a wa mafuta wa paefa.

6. Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi ana a nkhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda cirema;

7. ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.

8. Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya ku khonde la cipata, naturuke njira yomweyo.

9. Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'madyerero oikika, iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumpoto kudzalambira, aturukire njira ya ku cipata ca kumwera; ndi iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumwera, aturukire njira ya ku cipata ca kumpoto; asabwerere njira ya cipata anadzeraco, koma aturukire m'tsogolo mwace.

10. Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo poturuka iwo aturukire pamodzi.

11. Ndi pamadyerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.

12. Ndipo kalonga akapereka copereka caufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa cipata coloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, monga umo amacitira tsiku la Sabata; atatero aturuke; ndipo ataturuka, wina atseke pacipata.

13. Uziperekanso kwa Yehova mwana wa nkhosa wa caka cimodzi akhale nsembe yopsereza wopanda cirema, tsiku ndi tsiku, m'mawa ndi m'mawa, uzimpereka.

14. Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusanganiza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 46