Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 45:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pamadyerero, ndi pokhala mwezi, ndi pamasabata; pa madyerero onse oikika a nyumba ya Israyeli; ndipo apereke nsembe yaucimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kucitira cotetezera nyumba ya Israyeli.

18. Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndipo uyeretse malo opatulika.

19. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo, naupake pa mphuthu za kacisi, ndi pa ngondya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za cipata ca bwalo lam'kati.

20. Tsiku lacisanu ndi ciwiri la mweziwo ucitire momwemo ali yense wolakwa ndi wopusa; motero mucitire kacisiyo comtetezera.

21. Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi, muzicita Paskha, madyerero a masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda cotupitsa.

22. Ndipo tsiku lomwelo kalonga adzikonzere yekha ndi anthu onse a m'dziko ng'ombe, ikhale ya nsembe yaucimo.

23. Ndipo masiku asanu ndi awiri a madyerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda cirema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yaucimo.

24. Nakonze nsembe yaufa, ku ng'ombe kukhale efa; ndi ku nkhosa yamphongo kukhale efa; ndi kuefa kukhale hini wa mafuta.

25. Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi, pamadyerero, acite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yaucimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 45