Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 44:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'cuuno mwao; asabvale m'cuuno kanthu kali konse kakucititsa thukuta.

19. Ndipo akaturukira ku bwalo lakunja, ku bwalo lakunja kuti anthu, azibvula zobvala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, nabvale zobvala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.

20. Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingosenga mitu yao.

21. Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa ku bwalo la m'katimo.

22. Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asacite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israyeli, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.

23. Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.

24. Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pa madyerero anga onse oikika; napatulikitse masabata anga.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 44