Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 44:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anandibweza njira ya ku cipata cakunja ca malo opatulika coloza kum'mawa, koma cinatsekedwa.

2. Ndipo Yehova anati kwa ine, Cipata ici citsekeke, cisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israyeli walowerapo; cifukwa cace citsekeke.

3. Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe ku njira ya ku khonde la cipata, naturukire njira yomweyi.

4. Atatero anamuka nane njira ya cipata ca kumpoto kukhomo kwa kacisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.

5. Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ace onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi maturukidwe ace onse a malo opatulika.

6. Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israyeli inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse;

7. popeza mwalowa nao acilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munatyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.

8. Ndipo simunasunga udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira mokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.

9. Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israyeli.

10. Koma Aleviwo anandicokera kumka kutariwo, posokera Israyeli, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.

11. Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira ku zipata za kacisi, ndi kutumikira m'kacisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera naime pamaso pao kuwatumikira.

12. Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala cokhumudwitsa ca mphulupulu ca nyumba ya Israyeli, cifukwa cace ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.

13. Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira nchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga ziri zonse zopatulikitsazo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazicita.

14. Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa kacisi kwa utumiki wace wonse, ndi zonse zakumacitika m'mwemo.

15. Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israyeli, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 44