Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 43:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Lamulo la kacisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ace onse pozungulira pace azikhala opatulikitsa. Taonani, limeneli ndi lamulo la kacisi.

13. Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi cikhato), tsinde lace likhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono, ndi mkuzi wace m'mphepete mwace pozungulira pace kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.

14. Ndi kuyambira kunsi kwace kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwace mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikuru mikono inai; ndi kupingasa kwace mkono.

15. Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto pa guwa padzaturuka nyanga zinai.

16. Ndi pamoto pa guwa, m'litali mwace mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwace khumi ndi iwiri, lampwamphwa mbali zace zinai.

17. Ndi phaka, m'litali mwace mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwace mikono khumi ndi inai ku mbali zace zinai; ndi mkuzi wace pozungulira pace mkono wa nusu, ndi tsinde lace mkono pozungulira pace, ndi makwerero ace aloza kum'mawa.

18. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 43