Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 43:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anamuka nane ku cipata coloza kum'mawa,

2. ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ace ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wace.

3. Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona ku mtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.

4. Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa m'kacisi kudzera njira ya cipata coloza kum'mawa.

5. Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane ku bwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu unadzaza kacisi.

6. Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali m'kacisi, naima nane munthu.

7. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wacifumu wanga, mpoponda ku mapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli kosatha; ndi nyumba ya Israyeli siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa cigololo cao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,

8. ndi kuika ciundo cao pafupi pa ciundo canga, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazicita; cifukwa cace ndinawatha mu mkwiyo wanga.

9. Ataye tsono cigololo cao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha.

10. Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israyeli kacisiyu, kuti acite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wace.

11. Ndipo ngati akacita manyazi nazo zonse anazicita, uwadziwitse maonekedwe a kacisiyu, ndi muyeso wace, ndi poturukira pace, ndi polowera pace, ndi malongosoledwe ace onse, ndi malemba ace onse, ngakhale maonekedwe ace onse, ndi malamulo ace onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ace onse, ndi malemba ace onse, nawacite.

12. Lamulo la kacisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ace onse pozungulira pace azikhala opatulikitsa. Taonani, limeneli ndi lamulo la kacisi.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 43