Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona ku mtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.