Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 40:17-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pamenepo analowa nane ku bwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.

18. Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wace wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi.

19. Pamenepo anayesa kupingasa kwace kuyambira pakhomo pace pacipata cakunsi, kufikira kumaso kwace kwa bwalo la m'kati kunja kwace, mikono zana kum'mawa, ndi kumpoto.

20. Ndi cipata ca bwalo lakunja coloza kumpoto anaciyesa m'litali mwace, ndi kupingasa kwace.

21. Ndi zipinda zace ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, ndi makhoma a pakati pace; ndi zidundumwa zace zinali monga mwa muyeso wa cipata coyambaco, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

22. Ndi mazenera ace, ndi zidundumwa zace, ndi akanjedza ace, anali monga mwa muyeso wa cipata coloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zace zinali pakhomo.

23. Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati, copenyana ndi cipata cinzace cakunja kumpoto, ndi ca kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata mikono zana.

24. Ndipo ananditsogolera kumka kumwela, ndipo taonani, panali cipata kumwela, nayesa makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi.

25. Ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

26. Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zace kumaso kwace; ndi pa nsanamira zace cakuno ndi cauko panali akanjedza.

27. Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati cakulozakumwela, nayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata kumwela mikono zana.

28. Pamenepo analowa nane pa cipata ca kumwela m'bwalo lam'kati, nayesa cipata ca kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;

29. ndi zipinda zace, ndi makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo; m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

30. Ndipo panali zidundumwa pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi awiri mphambu isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu.

31. Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja, ndi pa nsanamira zace panali akanjedza, ndi pokwererapo panali makwerero asanu ndi atatu.

32. Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa cipata ca kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi;

33. ndi zipindazace, ndi makhoma a pakati pace, Indi zikundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

34. Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 40