Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 37:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira ciriri, gulu la nkhondo lalikurukuru ndithu.

11. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israyeli; taonani, akuti, Mafupa athu auma, ciyembekezo cathu catayika, talikhidwa.

12. Cifukwa cace, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu muturuke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israyeli.

13. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine. Yehova potsegula Ine kumanda kwanu, ndi kukweza inu kukuturutsani m'manda mwanu, anthu anga inu.

14. Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m'dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kucicita, ati Yehova.

15. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

16. Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israyeli anzace; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efraimu, ndi wa nyumba yonse ya Israyeli anzace;

17. nuiphatikize wina ndi unzace ikhale mtengo umodzi m'dzanja lako.

18. Ndipo ana a anthu amtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi?

19. unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efraimu, ndi wa mafuko a Israyeli anzace, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.

20. Ndipo mitengo imene ulembapo idzakhala m'dzanja mwako pamaso pao.

21. Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israyeli pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa ku mbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;

22. ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israyeli; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 37