Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 28:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.

15. Unali wangwiro m'njira zako cilengedwere iwe, mpaka cinapezeka mwa iwe cosalungama.

16. Mwa kucuruka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi ciwawa, ndipo unacimwa; cifukwa cace ndinakukankha kukucotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukucotsa pakati pa miyala yamoto.

17. Unadzikuza mtima cifukwa ca kukongola kwako, waipsa nzeru zako; cifukwa ca kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.

18. Mwa mphulupulu zako zocuruka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; cifukwa cace ndaturutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.

19. Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka coopsa, ndipo sudzakhalanso konse.

20. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

21. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Zidoni, nuunenere;

22. uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Zidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakucita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu.

23. Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ace, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwace ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

24. Ndipo nyumba ya Israyeli siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya ali yense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

25. Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israyeli mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwa iwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwao mwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga.

26. Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kunka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 28