Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 17:8-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Unaokedwa mu nthaka yabwino kuli madzi ambiri, kuti uphuke nthambi, nubale zipatso, nukhale mpesa wabwino.

9. Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? sadzausula ndi kudula zipatso zace, kuti uume, kuti masamba ace onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikuru, kapena anthu ambiri akuuzula?

10. Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? sudzauma ciumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? udzauma pookedwa apo udaphuka.

11. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti.

12. Uziti tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nciani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babulo inadza ku Yerusalemu, nitenga mfumu yace ndi akalonga ace, nibwera nao kuti iye ku Babulo;

13. nitenga wa mbumba yacifumu, nicita naye pangano, nimlumbiritsa, nicotsa amphamvu a m'dziko;

14. kuti ufumuwo ukhale wopepuka, kuti usadzikweze, koma kuti pakusunga pangano lace ukhale.

15. Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yace ku Aigupto, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? adzapulumuka wakucita izi? atyole pangano ndi kupulumuka kodi?

16. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamcititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lace, imene anatyola pangano lace, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babulo.

17. Ndipo Farao ndi nkhondo yace yaikuru, ndi khamu lace launyinji, sadzacita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.

18. Pakuti anapepula lumbiro, ndi kutyola pangano, angakhale anapereka dzanja lace; popeza anacita izi zonse sadzapulumuka.

19. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analityola, ndidzawabweza pamutu pace.

20. Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babulo, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwace anandilakwira nako.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 17