Panalinso ciombankhanga cina cacikuru, ndi mapiko akuru, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unacipindira mizu yace, nucilunjikitsira nthambi zace, kucokera pookedwa pace, kuti ciuthirire madzi.