Ndipo Farao ndi nkhondo yace yaikuru, ndi khamu lace launyinji, sadzacita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.