Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 9:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israyeli, ndi ansembe, ndi Alevi, sanadzilekanitsa ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amoabu, Aaigupto, ndi Aamori.

2. Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.

3. Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba cobvala canga, ndi maraya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndebvu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.

4. Nandisonkhanira ali yense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israyeli, cifukwa ca kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.

5. Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, cobvala canga ndi maraya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;

Werengani mutu wathunthu Ezara 9