Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 8:24-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Pamenepo ndinapatula akulu a ansembe khumi ndi awiri, ndiwo Serebiya, Hasabiya, ndi abale ao khumi pamodzi nao,

25. ndi kuwayesera siliva, ndi golidi, ndi zipangizo, ndizo copereka ca kwa nyumba ya Mulungu wathu, cimene mfumu, ndi aphungu ace, ndi akalonga ace, ndi Aisrayeli onse anali apawa, adapereka.

26. Ndipo ndinawayesera m'dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi,

27. ndi zikho zagolidi makumi awiri za madariki cikwi cimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golidi.

28. Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golidi, ndizo copereka caufulu ca kwa Yehova Mulungu wa makolo anu.

29. Mukhale maso ndi kuzisunga mpaka muziyesera pamaso pa akulu a ansembe ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo a Israyeli ku Yerusalemu, m'zipinda za nyumba ya Yehova.

30. Potero ansembe ndi Alevi analandira kulemera kwace kwa siliva ndi golidi ndi zipangizo, abwere nazo ku Yerusalemu ku nyumba ya Mulungu wathu.

31. Pamenepo tinacoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi ciwiri la mwezi woyamba, kumka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira.

32. Ndipo tinafika ku Yerusalemu ndi kukhalako masiku atatu.

33. Ndi pa tsiku lacinai siliva ndi golidi ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uliya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Pinehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadia mwana wa Binui, Alevi;

34. zonsezi anaziwerenga ndi kuziyesa; ndi kulemera kwace konse kunalembedwa nthawi yomweyo.

35. Otengedwa ndende, ataturuka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israyeli, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisrayeli onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, ana a nkhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezara 8