Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golidi, ndizo copereka caufulu ca kwa Yehova Mulungu wa makolo anu.