Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 8:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israyeli; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ace ndi abale ace khumi mphambu asanu ndi atatu;

19. ndi Hasabiya, ndi pamodzi naye Yesaya wa ana a Merari, abale ace ndi ana ao makumi awiri;

20. ndi a Anetini, amene Davide ndi akalonga adapereka atumikire Alevi, Anetini mazana awiri mphambu makumi awiri, onsewo ochulidwa maina.

21. Pamenepo ndinalalikira cosala komweko ku mtsinje wa Ahava, kuti tidzicepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi cuma cathu conse.

22. Pakuti ndinacita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikari, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yace ndi mkwiyo wace zitsutsana nao onse akumsiya.

23. Momwemo tinasala ndi kupempha ici kwa Mulungu wathu; natibvomereza Iye,

24. Pamenepo ndinapatula akulu a ansembe khumi ndi awiri, ndiwo Serebiya, Hasabiya, ndi abale ao khumi pamodzi nao,

25. ndi kuwayesera siliva, ndi golidi, ndi zipangizo, ndizo copereka ca kwa nyumba ya Mulungu wathu, cimene mfumu, ndi aphungu ace, ndi akalonga ace, ndi Aisrayeli onse anali apawa, adapereka.

26. Ndipo ndinawayesera m'dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi,

27. ndi zikho zagolidi makumi awiri za madariki cikwi cimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golidi.

28. Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golidi, ndizo copereka caufulu ca kwa Yehova Mulungu wa makolo anu.

Werengani mutu wathunthu Ezara 8