Pamenepo ndinalalikira cosala komweko ku mtsinje wa Ahava, kuti tidzicepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi cuma cathu conse.